ZEKARIYA10nya_bib

Yehova Adzasamalira Yuda

1Pemphani mvula kwa Yehova pa nthawi yamphukira;ndi Yehova amene amapanga mitambo ya mvula.Iye amagwetsa mivumbi ya mvula kwa anthu,ndi kumeretsa mbewu za mʼmunda kwa aliyense.2Mafano amayankhula zachinyengo,owombeza mawula amaona masomphenya abodza;amafotokoza maloto onama,amapereka chitonthozo chopandapake.Choncho anthu amangoyendayenda ngati nkhosa zozunzikachifukwa chosowa mʼbusa.
3“Ine ndawakwiyira kwambiri abusa,ndipo ndidzalanga atsogoleri;pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzasamalirankhosa zake, nyumba ya Yuda,ndi kuwasandutsa ngati akavalo aulemerero ankhondo.4Mu Yuda mudzachokera mwala wapangodya,mudzachokera chikhomo cha tenti,mudzachokera uta wankhondo,mudzachokera mtsogoleri aliyense.5Onse pamodzi adzakhala ngati ngwazi zankhondozoponda mʼmatope a mʼmisewu nthawi yankhondo.Chifukwa Yehova adzakhala nawo,adzachita nkhondo ndi kugonjetsa okwera pa akavalo.
6“Ndidzalimbitsa nyumba ya Yudandi kupulumutsa nyumba ya Yosefe.Ndidzawabwezeretsachifukwa ndawamvera chisoni.Adzakhala ngati kutisindinawakane,chifukwa ndine Yehova Mulungu wawondipo ndidzawayankha.7Aefereimu adzakhala ngati ankhondo amphamvuadzasangalala ngati anthu amene amwa vinyo.Ana awo adzaziona zimenezi ndipo adzasangalala;mʼmitima mwawo adzakondwa mwa Ambuye.8Ndidzaliza mluzundi kuwasonkhanitsa pamodzi.Ndithu ndawawombola;adzachulukana ngati poyamba paja.9Ndinawamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu,koma ku mayiko akutaliwo adzandikumbukira.Iwo pamodzi ndi ana awo adzapulumuka,ndipo adzabwerera.10Ndidzawabweretsa kuchokera ku Iguptondipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya.Ndidzawabwezera ku Giliyadi ndi ku Lebanoni,mpaka malo woti nʼkukhalamo adzatheratu.11Adzawoloka nyanja ya masautso;nyanja yokokoma idzagonjandipo madzi onse a mu Nailo adzaphwa.Kudzikuza kwa Asiriya kudzathandipo ndodo yaufumu ya Igupto idzathyoka.12Ndidzalimbitsa iwo mwa Yehovandipo adzayenda mʼdzina lake,”akutero Yehova.