MASALIMO88nya_bib

Salimo la ana a Kora. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a nyimbo yoti: “Pa Matenda ndi pa Mazunzo.” Ndakatulo ya Hemani, wa banja la Ezara.

1Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa,usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.2Pemphero langa lifike pamaso panu;tcherani khutu lanu kuti mumve kulira kwanga.
3Pakuti ndili ndi mavuto ambirindipo moyo wanga ukuyandikira ku manda.4Ndikuwerengedwa pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje;ndine munthu wopanda mphamvu.5Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa,monga ophedwa amene agona mʼmanda,amene Inu simuwakumbukiranso,amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.
6Mwandiyika pansi pa dzenje penipeni,mʼmalo akuya a mdima waukulu.7Ukali wanu ukundipsinja kwambiri,mwandiopseza kwambiri ndi mafunde anu onse.Sela8Mwandichotsa pakati pa abwenzi anga enienindipo mwachititsa kuti ndikhale chonyansa kwa iwo.Ndatsekerezedwa ndipo sindingathe kuthawa;9maso anga ada ndi chisoni.Ndimayitana Inu Yehova tsiku lililonse;ndimakweza manja anga kwa Inu.10Kodi mumaonetsa zozizwitsa zanu kwa anthu akufa?Kodi iwo amene afa amaukanso ndi kutamanda Inu?Sela11Kodi chikondi chanu chimalalikidwa mʼmanda,za kukhulupirika kwanu ku malo a chiwonongeko?12Kodi zozizwitsa zanu zimadziwika ku malo a mdima,kapena ntchito zanu zolungama ku dziko la anthu oyiwalika?
13Inu Yehova, Ine ndimalirira thandizo;mmawa mapemphero anga amafika pamaso panu.14Inu Yehova nʼchifukwa chiyani mukundikanandi kundibisira nkhope yanu?
15Kuyambira ubwana wanga ndakhala ndikuzunzika pafupi kufa;ndakhala ndikuchita mantha ndipo ndine wothedwa nzeru.16Ukali wanu wandimiza;zoopsa zanu zandiwononga.17Tsiku lonse zimandizungulira ngati chigumula;zandimiza kwathunthu.18Inu mwatenga anzanga ndi okondedwa anga kuwachotsa pamaso panga;mdima ndiye bwenzi langa lenileni.