MASALIMO87nya_bib

Salimo la Ana a Kora.

1Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;2Yehova amakonda zipata za Ziyonikupambana malo onse okhalamo a Yakobo.3Za ulemerero wako zimakambidwa,Iwe mzinda wa Mulungu:Sela4“Ndidzanena za Rahabe ndi Babulonipakati pa iwo amene amandidziwa.Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”
5Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,“Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”6Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:“Uyu anabadwira mʼZiyoni.”Sela7Oyimba ndi ovina omwe adzati,“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”