MASALIMO84nya_bib
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora.
1Malo anu okhalamo ndi okomadi,Inu Yehova Wamphamvuzonse!2Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,kufuna mabwalo a Yehova;Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwuliraMulungu wamoyo.3Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo,ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa,kumene amagonekako ana akepafupi ndi guwa lanu la nsembe,Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.4Odala amene amakhala mʼNyumba yanu;nthawi zonse amakutamandani.Sela5Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu,mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.6Pamene akudutsa chigwa cha Baka,amachisandutsa malo a akasupe;mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.7Iwo amanka nakulirakulira mphamvumpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.8Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse;mvereni Inu Mulungu wa Yakobo.Sela9Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu;yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.10Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzikuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wangakuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.11Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;Iye sawamana zinthu zabwinoiwo amene amayenda mwangwiro.12Inu Yehova Wamphamvuzonse,wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.