MASALIMO6nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.

1Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,kapena kundilanga mu ukali wanu.2Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.3Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
4Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.5Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;Amakutamandani ndani ali ku manda?
6Ine ndatopa ndi kubuwula;usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.7Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
8Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,pakuti Yehova wamva kulira kwanga.9Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;Yehova walandira pemphero langa.10Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.