MASALIMO51nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba.

1Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;molingana ndi chifundo chanu chachikulumufafanize mphulupulu zanga.2Munditsuke zolakwa zanga zonsendipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.
3Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga,ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.4Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwandipo ndachita zoyipa pamaso panu,Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungamapamene muyankhula ndi pamene muweruza.5Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa,wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.6Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga;mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.
7Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera,munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala8Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.9Mufulatire machimo angandi kufafaniza zolakwa zanga zonse.
10Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungundi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.11Musandichotse pamaso panukapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.12Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanundipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.
13Pamenepo ndidzaphunzitsa anthu amphulupulu njira zanukuti ochimwa adzabwerere kwa inu.14Mundipulumutse ku tchimo lokhetsa magazi, Inu Mulungu,Mulungu wa chipulumutso changa,ndipo lilime langa lidzayimba zachilungamo chanu.15Inu Ambuye tsekulani milomo yanga,ndipo pakamwa panga padzalengeza matamando anu.16Inu simusangalatsidwa ndi nsembe wamba.Ndikanapereka nsembe yopsereza, Inu simukondwera nayo.17Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka;mtima wosweka ndi wachisoniInu Mulungu simudzawunyoza.
18Mwa kukoma mtima kwanu mupange Ziyoni kuti alemere;mumange makoma a Yerusalemu.19Kotero kudzakhala nsembe zachilungamo,nsembe yonse yopsereza yokondweretsa Inu;ndipo ngʼombe zazimuna zidzaperekedwa pa guwa lanu la nsembe.