MASALIMO23nya_bib
Salimo la Davide.
1Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.2Amandigoneka pa msipu wobiriwira,amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,3amatsitsimutsa moyo wanga.Amanditsogolera mʼnjira zachilungamochifukwa cha dzina lake.4Ngakhale ndiyendemʼchigwa cha mdima wakuda bii,sindidzaopa choyipa,pakuti Inu muli ndi ine;chibonga chanu ndi ndodo yanuzimanditonthoza.5Mumandikonzera chakudyaadani anga akuona.Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;chikho changa chimasefukira.6Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsatamasiku onse a moyo wanga,ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehovakwamuyaya.