MASALIMO140nya_bib
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
1Landitseni Yehova kwa anthu oyipa;tetezeni kwa anthu ankhanza,2amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipandi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse.3Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka;pa milomo yawo pali ululu wa mamba.Sela4Tetezeni Inu Yehova, kwa anthu oyipa;tchinjirizeni kwa anthu ankhanzaamene amakonza zokola mapazi anga.5Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika;iwo atchera zingwe za maukonde awondipo anditchera misampha pa njira yanga.Sela6Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.”Imvani kupempha kwanga Yehova.7Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu,mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.8Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova;musalole kuti zokonza zawo zitheke,mwina iwo adzayamba kunyada.Sela9Mitu ya amene andizunguliraiphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.10Makala amoto agwere pa iwo;aponyedwe pa moto,mʼmaenje amatope, asatulukemonso.11Musalole kuti anthu achipongwe akhazikike mʼdziko;choyipa chilondole anthu ankhanza.12Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka,ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.13Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu,ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.