PSA131nya_bib
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Davide.
1Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza,maso anga siwonyada;sinditengeteka mtimandi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.2Koma moyo wanga ndawutontholetsandi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa,moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa.3Yembekeza Yehova, iwe Israeli,kuyambira tsopano mpaka muyaya.