MASALIMO130nya_bib

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;2Ambuye imvani mawu anga.Makutu anu akhale tcheru kumvakupempha chifundo kwanga.
3Inu Yehova, mukanamawerengera machimo,Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?4Koma kwa Inu kuli chikhululukiro;nʼchifukwa chake mumaopedwa.
5Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera,ndipo ndimakhulupirira mawu ake.6Moyo wanga umayembekezera Ambuye,kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
7Yembekeza Yehova, iwe Israeli,pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthikandipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.8Iye mwini adzawombola Israeliku machimo ake onse.