MASALIMO128nya_bib
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
1Odala ndi onse amene amaopa Yehova,amene amayenda mʼnjira zake.2Udzadya chipatso cha ntchito yako;madalitso ndi chuma zidzakhala zako.3Mkazi wako adzakhala ngati mpesa woberekamʼkati mwa nyumba yako;ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivikuzungulira tebulo lako.4Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwaamene amaopa Yehova.5Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyonimasiku onse a moyo wako;uwone zokoma za Yerusalemu,6ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.Mtendere ukhale ndi Israeli.