MASALIMO125nya_bib
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
1Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni,limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.2Monga mapiri azungulira Yerusalemu,momwemonso Yehova azungulira anthu akekuyambira tsopano mpaka muyaya.3Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhalapa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama,kuti anthu olungamawoangachite nawonso zoyipa.4Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino,amene ndi olungama mtima5Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota,Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa.Mtendere ukhale pa Israeli.