MASALIMO111nya_bib
1Tamandani Yehova.Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonsemʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.2Ntchito za Yehova nʼzazikulu;onse amene amakondwera nazo amazilingalira.3Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu,ndipo chilungamo chake ndi chosatha.4Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike;Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.5Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye;amakumbukira pangano lake kwamuyaya.6Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake,kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.7Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama;malangizo ake onse ndi odalirika.8Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi,ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.9Iyeyo amawombola anthu ake;anakhazikitsa pangano lake kwamuyayadzina lake ndi loyera ndi loopsa.10Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.