MASALIMO11nya_bib
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
1Mwa Yehova ine ndimathawiramo.Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti,“Thawira ku phiri lako ngati mbalame.2Pakuti taona oyipa akunga mauta awo;ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta,pobisala pawo kuti alaseolungama mtima.3Tsono ngati maziko awonongeka,olungama angachite chiyani?”4Yehova ali mʼNyumba yake yoyera;Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba.Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu;maso ake amawayesa.5Yehova amayesa olungama,koma moyo wake umadana ndi oyipa,amene amakonda zachiwawa.6Iye adzakhuthulira pa oyipamakala amoto ndi sulufule woyaka;mphepo yotentha idzakhala yowayenera.7Pakuti Yehova ndi wolungama,Iye amakonda chilungamo;ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.