MIYAMBO
9
/
nya_bib
Za Nzeru ndi Uchitsiru
1
Nzeru inamanga nyumba yake;
inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.
2
Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake;
inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.
3
Nzeruyo inatuma adzakazi ake,
kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,
4
“Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!”
Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,
5
“Bwerani, dzadyeni chakudya changa
ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.
6
Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo;
yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.”
7
Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo;
aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.
8
Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe;
dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.
9
Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru;
ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.
10
Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru;
kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.
11
Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka,
ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.
12
Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa;
ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.
13
Uchitsiru ndi mkazi waphokoso,
wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.
14
Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake,
pamalo aatali a mu mzinda,
15
kuti aziyitana anthu ongodutsa,
amene akunka nayenda njira zawo.
16
Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,”
ndipo kwa wopanda nzeru amati,
17
“Madzi akuba ndiye amatsekemera;
chakudya chodya mobisa ndi chokoma!”
18
Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko,
ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya.
Powered by Seed Bible API
expand_more
Search
All books
Old Testament
New Testament
chevron_left
Previous Chapter
Books
search
Search
explore
Discover
share
Share
chevron_right
Next Chapter