NUMERI24nya_bib
1Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu.2Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye3ndipo ananena uthenga wake:“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka,4uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere:5“Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo,misasa yako, iwe Israeli!6“Monga zigwa zotambalala,monga minda mʼmbali mwa mtsinje,monga aloe wodzalidwa ndi Yehova,monga mikungudza mʼmbali mwa madzi.7Madzi adzayenderera mʼmitsuko yake;mbewu zake zidzakhala ndi madzi ambiri.“Mfumu yake idzakhala yamphamvu kuposa Agagi;ufumu wake udzakwezedwa.8“Mulungu womutulutsa mʼdziko la Iguptoali ndi mphamvu ngati za njati.Amawononga mitundu yomuwukirandi kuphwanya mafupa awo,amalasa ndi mivi yake.9Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi,monga mkango waukazi, adzamuputa ndani?“Amene adalitsa iwe, adalitsikendipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”10Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka.11Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”12Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine,13kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena?14Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.”