NUMERI13nya_bib
Kukazonda Kanaani
1Yehova anawuza Mose kuti,2“Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.”3Monga mwa mawu a Yehova, Mose anawatuma kuchokera ku chipululu cha Parani. Onsewo anali atsogoleri a Aisraeli.4Mayina awo ndi awa:kuchokera ku fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri;5kuchokera ku fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori;6kuchokera ku fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune;7kuchokera ku fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe;8kuchokera ku fuko la Efereimu, Hoseya mwana wa Nuni;9kuchokera ku fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu;10kuchokera ku fuko la Zebuloni, Gadieli mwana wa Sodi;11kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi;12kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali;13kuchokera ku fuko la Aseri, Seturi mwana wa Mikayeli;14kuchokera ku fuko la Nafutali, Naabi mwana wa Vofisi;15kuchokera ku fuko la Gadi, Geuweli mwana wa Maki.16Amenewa ndiwo mayina a anthu amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo. (Hoseya mwana wa Nuni, Mose anamupatsa dzina loti Yoswa).17Mose atawatuma kuti akazonde Kanaani anati, “Mupite kudzera ku Negevi, mukapitirire mpaka ku dziko la mapiri.18Mukaone dzikolo kuti ndi lotani ndi anthu okhala mʼmenemo ngati ndi amphamvu kapena ofowoka, ochepa kapena ambiri.19Nanga dziko limene akukhalako ndi lotani? Ndi labwino kapena loyipa? Mizinda imene akukhalamo ndi yotani? Kodi ilibe malinga kapena ndi ya malinga?20Nthaka yake ndi yotani? Yachonde kapena yopanda chonde? Kodi dzikolo lili ndi mitengo kapena lilibe mitengo? Mukayesetse kubweretsako zipatso za mʼdzikomo.” (Inali nthawi yamphesa zoyamba kupsa).21Choncho anapita kukazonda dzikolo kuchokera ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu, mopenyana ndi Lebo Hamati.22Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto).23Atafika ku chigwa cha Esikolo, anadulako nthambi ya mpesa ya phava limodzi la mphesa ndipo anthu awiri ananyamulizana, natenganso makangadza ndi nkhuyu.24Malo amenewo anawatcha chigwa cha Esikolo chifukwa cha phava la mphesa limene Aisraeli anadula kumeneko.25Patapita masiku makumi anayi, anthu aja anabwerako kokazonda dziko lija.