MIKA5nya_bib

Wolamulira Wochokera ku Betelehemu

1Iwe mzinda wa anthu ankhondo, sonkhanitsa anthu ako ankhondo,pakuti anthu atizungulira kuti alimbane nafe.Adzakantha ndi ndodo pa chibwanocha wolamulira wa Israeli.
2“Koma iwe Betelehemu Efurata,ngakhale uli wonyozeka pakati pa mafuko a Yuda,mwa iwe mudzatulukamunthu amene adzalamulira Israeli,amene chiyambi chake nʼchakalekale,nʼchamasiku amakedzana.”
3Nʼchifukwa chake Israeli adzasiyidwampaka pa nthawi imene mayi amene ali woyembekezera adzachire.Ndipo abale ake onse otsalira adzabwererakudzakhala pamodzi ndi Aisraeli.
4Iye adzalimbika, ndipo adzaweta nkhosa zakemwa mphamvu ya Yehova,mu ulemerero wa dzina la Yehova Mulungu wake.Ndipo iwo adzakhala mu mtendere,pakuti ukulu wake udzakhala ponseponse pa dziko lapansi.5Ndipo Iye adzakhala mtendere wawo.Chipulumutso ndi ChiwonongekoAsiriya akadzalowa mʼdziko lathundi kuyamba kuthira nkhondo malo athu otetezedwa,tidzawadzutsira abusa asanu ndi awiri,ngakhalenso atsogoleri asanu ndi atatu.6Iwo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga,dziko la Nimurodi adzalilamulira mwankhondo.Adzatipulumutsa kwa Asiriyaakadzafika mʼmalire a mʼdziko lathukudzatithira nkhondo.
7Otsalira a Yakobo adzakhalapakati pa mitundu yambiri ya anthungati mame ochokera kwa Yehova,ngati mvumbi pa udzu,omwe sulamulidwa ndi munthukapena kudikira lamulo la anthu.8Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu,mʼgulu la anthu a mitundu yambiri,ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango.Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa,amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula,ndipo palibe angathe kuzilanditsa.9Mudzagonjetsa adani anu,ndipo adani anu onse adzawonongeka.10Yehova akuti,“Tsiku limenelo ndidzawononga akavalo anu onsendi kuphwasula magaleta anu.11Ndidzawononga mizinda ya mʼdziko mwanundi kugwetsa malinga anu onse.12Ndidzawononga ufiti wanundipo sikudzakhalanso anthu owombeza mawula.13Ndidzawononga mafano anu osemapamodzi ndi miyala yanu yopatulika imene ili pakati panu;simudzagwadiranso zinthu zopangandi manja anu.14Ndidzazula mitengo ya mafano a Asera imene ili pakati panu,ndipo ndidzawononga mizinda yanu.15Ndidzayilanga mwaukali ndi mokwiyamitundu imene sinandimvere Ine.”