YEREMIYA49nya_bib
Uthenga Wonena za Aamoni
1Yehova ananena izi:Amoni,“Kodi Israeli alibe ana aamuna?Kapena alibe mlowamʼmalo?Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi?Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?2Koma nthawi ikubwera,”akutero Yehova,“pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondoku Raba, likulu la Amoni;ndipo malo awo opembedzera milungu yawoadzatenthedwa ndi moto.Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawokuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,”akutero Yehova.3“Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika!Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba!Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu;thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga,chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo,pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.4Chifukwa chiyani mukunyadirachigwa chanu,inu anthu osakhulupirikaamene munadalira chuma chanu nʼkumati:‘Ndani angandithire nkhondo?’5Ndidzabweretsa zoopsa pa iwezochokera kwa onse amene akuzungulira,”akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse.“Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake.Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo.6“Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,”akutero Yehova.