YEREMIYA4nya_bib
1“Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli,bwererani kwa Ine,”akutero Yehova.“Chotsani mafano anu onyansa pamaso pangandipo musasocherenso.2Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamokuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitsendipo adzanditamanda.”3Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi:“Limani masala anumusadzale pakati pa minga.4Dziperekeni nokha kwa Inekuti munditumikire ndi mtima wanu wonse,inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu.Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani,chifukwa cha ntchito zanu zoyipazopopanda wina wowuzimitsa.