YEREMIYA3nya_bib
1“Ngati munthu asudzula mkazi wakendipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina,kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo?Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri?Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri.Komabe bwerera kwa ine,”akutero Yehova.2“Tayangʼana ku zitunda zowuma.Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama?Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako,ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu.Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanundi ntchito zanu zoyipa.3Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula,ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe.Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere;ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe.4Kodi iwe siposachedwa pomwepa pamene wanenakuti, ‘Abambo anga, Inu bwenzi langa la unyamata wanga,5kodi mudzandikwiyira nthawi zonse?Kodi ukali wanu udzakhalabe mpaka muyaya?’Umu ndimo mmene umayankhulira,koma umapitirizabe kuchita zoyipa monga momwe umathera.”