YEREMIYA17nya_bib
1“Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi.Uchimowo walembedwa pa mitima yawondiponso pa nyanga za maguwa awo.2Ngakhale ana awo amakumbukiramaguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera,pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri,pa mapiri aatali mʼdzikomo.3Chuma chanu ndiponso katundu wanu yensendidzazipereka kwa ofunkhakuti zikhale dipo lawochifukwa cha machimoochitika mʼdziko lonse.4Mudzataya dziko limene ndinakupatsanikuti likhale cholowa chanu.Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anumʼdziko limene inu simukulidziwa,chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto,ndipo udzayaka mpaka muyaya.”5Yehova akuti,“Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake,amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandizepamene mtima wake wafulatira Yehova.6Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu;iye sadzapeza zabwino.Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi,mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.7“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,amene amatsamira pa Iye.8Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madziumene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje.Mtengowo suopa pamene kukutentha;masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse.Suchita mantha pa chaka cha chilalandipo sulephera kubereka chipatso.”9Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonsendipo kuyipa kwake nʼkosachizika.Ndani angathe kuwumvetsa?10“Ine Yehova ndimafufuza mtimandi kuyesa maganizo,ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe akendiponso moyenera ntchito zake.”11Munthu amene amapeza chuma mwachinyengoali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire.Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera,ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.12Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemererowokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.13Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli,onse amene amakusiyani adzachita manyazi.Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbichifukwa anakana Yehova,kasupe wa madzi amoyo.14Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.15Anthu akumandinena kuti,“Mawu a Yehova ali kuti?Zichitiketu lero kuti tizione!”16Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange.Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka.Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.17Musandichititse mantha;ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto.18Ondizunza anga achite manyazi,koma musandichititse manyazi;iwo achite mantha kwambiri,koma ine mundichotsere manthawo.Tsiku la mavuto liwafikire;ndipo muwawononge kotheratu.