YESAYA57nya_bib
1Anthu olungama amafa,ndipo palibe amene amalingalira mu mtima mwake;anthu odzipereka amatengedwa,ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake.Anthu olungama amatengedwakuti tsoka lisawagwere.2Iwo amene amakhala moyo wolungamaamafa mwamtendere;amapeza mpumulo pamene agona mu imfa.3“Bwerani kuno, anthu ochita zoyipa,inu muli ngati zidzukulu za mkazi wachigololo ndi wadama!4Kodi inu mukuseka yani?Kodi mukumunena ndanindi kupotoza pakamwa panu?Kodi inu si ana owukira,zidzukulu za anthu abodza?5Inu mumapembedza mafano pamene mumalobodoka ndi zilakolako zanu pakati pa mitengo ya thundu,ndiponso pa tsinde pa mtengo uliwonse wa nthambi zambiri.Mumapereka ana anu ngati nsembe mu zigwandiponso mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.6Mafano a pakati pa miyala yosalala ya mu zigwa ndiye chuma chanu. Inde, ndiye gawo lanu.Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa mafanowo,ndipo mumaperekanso chopereka cha chakudya.Kodi zimenezizingandichititse kuti ndikukomereni mtima?7Inu munayiwala bedi lanu pa phiri lalitali ndi looneka kutali.Mumapita kumeneko kukapereka nsembe zanu.8Mʼnyumba mwanu mwayikamafano kuseri kwa zitseko ndiponso pa mphuthu.Mwandisiya Ine, mwavula zovala zanu.Bedi lanu mwalikulitsa ndipo mwakwera ndi zibwenzi zanu,ndiye mwazilipira kuti mugone nazo.Kumene mwakwaniritsa zilakolako zanu zoyipa.9Mumapita kukapembedza fano la Moleki mutatenga mafutandi zonunkhira zochuluka.Munachita kutumiza akazembe anu kutali;inu ngakhale munapita ku manda kwenikweniko!10Inu mumatopa ndi maulendo anu,koma simunathe kunena kuti, ‘Nʼzopanda phindu.’Munapezako kumeneko zokhumba zanunʼchifukwa chake simunalefuke.11“Kodi ndani amene mwachita naye mantha ndi kumuopa,kotero kuti mwakhala mukundinamiza,ndipo Ine simundikumbukira nʼkomwe,kapena kuganizirapo mʼmitima yanu za Ine?Kodi mwaleka kundiopa chifukwa chotindakhala chete nthawi yayitali?12Koma ndaonetsa poyera ntchito zanu zomwe mumati nʼzolungama,ndi mafano anu kuti nʼzosathandiza.13Pamene mufuwula kupempha thandizo,mafano anu amene munasonkhanitsawo ndiyetu akupulumutseni!Mphepo idzanyamula mafano anu onsewo,mpweya chabe udzawulutsa mafanowo.Koma munthu amene amadalira ineadzalandira dziko lokhalamo.Phiri langa lopatulika lidzakhala lakelake.”