YESAYA15nya_bib

Za Kulangidwa kwa Mowabu

1Uthenga wonena za Mowabu:Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa,wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.Mzinda wa Kiri wawonongedwa,wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.2Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo,akupita ku malo awo achipembedzo kukalira;anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba.Mutu uliwonse wametedwa mpala,ndipo ndevu zonse zametedwa.3Mʼmisewu akuvala ziguduli;pa madenga ndi mʼmabwaloaliyense akulira mofuwula,misozi ili pupupu.4Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula,mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi.Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula,ndipo ataya mtima.
5Inenso ndikulirira Mowabu;chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowarindi Egilati-Selisiyaakupita akulira ku chikweza cha Luhiti,Akulira mosweka mtimapa njira yopita ku Horonaimu;akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo.6Madzi a ku Nimurimu aphwandipo udzu wauma;zomera zawonongekandipo palibe chomera chobiriwira chatsala.7Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga,achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi.8Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu;kulira kwawo kosweka mtima kukumvekampaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu.9Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi,komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni,mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabundi aliyense wotsala mʼdzikomo.