GENESIS37nya_bib
Maloto a Yosefe
1Yakobo ankakhala mʼdziko la Kanaani kumene abambo ake ankakhala.2Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi:Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake.3Tsono Israeli ankakonda Yosefe koposa ana ake ena onse, chifukwa anali mwana wobadwa muukalamba wake. Ndipo anamusokera mkanjo wa manja aatali.4Pamene abale ake anaona kuti abambo awo ankakonda Yosefe kuposa aliyense wa iwo, anayamba kumuda Yosefe ndipo sankayankhula naye zamtendere.5Tsiku lina Yosefe analota maloto ndipo pamene anawuza abale ake za malotowo, iwo anawonjeza kumuda.6Iye anawawuza kuti, “Tamvani maloto amene ndinalota:7Ife timamanga mitolo ya tirigu ku munda ndipo mwadzidzidzi mtolo wanga unayimirira chilili, pamene mitolo yanu inazungulira mtolo wangawo nʼkumawugwadira.”8Abale ake aja anamufunsa nati, “Kodi ukuyesa kuti ungakhale mfumu yathu? Ungadzatilamuliredi iweyo?” Ndipo anamuda kuposa kale chifukwa cha maloto ake ndi zimene ankakonda kunena kwa abambo awo.9Tsiku lina analotanso maloto ena, ndipo anafotokozera abale ake za malotowo. Iye anati, “Tamverani, ndinalotanso maloto ena. Ulendo uno dzuwa ndi mwezi pamodzi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zimandigwadira.”10Atawuza abambo ake ndi abale ake malotowa, abambo ake anamukalipira nati, “Ndi maloto anji umalotawa? Kodi uganiza kuti ine, amayi ako pamodzi ndi abale ako onsewa tingadzabwere kudzakugwandira iwe?”11Abale ake anamuchitira nsanje, koma abambo ake anasunga nkhaniyi mu mtima.