EZARA6nya_bib
Lamulo la Mfumu Dariyo
1Atalandira mawuwo mfumu Dariyo anapereka lamulo ndipo kafukufuku anachitikadi ku Babuloni mʼnyumba yosungira chuma ndi mabuku ambiri yakale.2Ndipo ku Ekibatana, likulu la dera la Mediya, kunapezeka mpukutu mmene munalembedwa kuti, Chikumbutso:3Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi, mfumuyo inapereka lamulo lokhudza Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu.Analamula kuti Nyumba ya Mulungu imangidwenso kukhala malo woperekerako nsembe. Maziko ake amangidwe kolimba pa malo pomwe paja pali maziko ake akale ndipo mulitali mwake mukhale mamita 27, mulifupi mwake mukhale mamita 27.4Mumange mizere itatu ya miyala yayikulu ndi mzere umodzi wa matabwa, ndalama zake zolipirira ntchitoyo zichokere mʼthumba la ufumu.5Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu kupita nazo ku Babuloni, zonsezi zibwezedwe ndipo zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake mʼNyumbayo.6Tsopano Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate ndiponso Setari-Bozenai pamodzi ndi anzanu muchokeko kumeneko.7Ntchito yomanga Nyumba ya Mulunguyi muyileke. Mulekeni bwanamkubwa wa Ayuda ndiponso akuluakulu a Ayuda kuti amangenso Nyumba ya Mulunguyo pamalo pake.8Kuwonjezera pamenepo, ndikukhazikitsa lamulo lonena za mmene mudzachitire ndi akuluakulu a Ayuda powathandiza kumanganso Nyumba ya Mulunguyo: Anthuwa muwalipire msanga kuchokera mʼthumba la ufumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate.9Ndipo zonse zofunikira monga, ana angʼombe, nkhosa zazimuna, ana ankhosa aamuna zoperekera nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba, ndi tirigu, mchere, vinyo ndi mafuta monga mmene ansembe a ku Yerusalemu angafunire, muziwapatsa zimenezo tsiku ndi tsiku ndipo musamalephere kutero.10Zikatero ndiye kuti azipereka nsembe za fungo lokomera Mulungu wakumwamba ndi kupempherera moyo wa mfumu ndi ana ake.11Ndikulamulanso kuti ngati wina asintha zimene ndalamulazi, mtanda umodzi wa nyumba yake udzasololedwa ndi kumunkhomera pamenepo ndipo nyumba yake adzayisandutse dzala.12Mulungu amene anasankha kuti anthu azimupembedza pa malo amenewa, achotse mfumu iliyonse kapena munthu aliyense amene adzasinthe zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemuko. Ine Dariyo ndikuyika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri.