3 YOHANE1nya_bib
1Ndine mkulu wampingo, kulembera: Gayo mnzanga wokondedwa, amene ndimamukonda mʼchoonadi.2Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu.3Ine ndinali ndi chimwemwe chachikulu pamene abale ena anafika nʼkundifotokozera za kukhulupirika kwako pa choonadi ndiponso mmene umayendera motsata choonadi.4Palibe chondikondweretsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akukhala mʼchoonadi.5Wokondedwa, ndiwe wokhulupirika pa zimene ukuchitira abale, ngakhale kuti iwowo ndi alendo.6Iwo anafotokozera mpingo za chikondi chako. Chonde uwathandize kupitiriza ulendo mʼnjira yokondweretsa Mulungu.7Pakuti ananyamuka ulendo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye, osalandira thandizo kwa osakhulupirira.8Ife tiyenera kumathandiza anthu oterewa, kuti tigwirizane nawo pa ntchito ya choonadi.