NYIMBO YA SOLOMONI5nya_bib

1Ndalowa mʼmunda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkwatibwi wanga;ndasonkhanitsa mure wanga ndi zokometsera zakudya zanga.Ndadya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe;ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.AbwenziIdyani abwenzi anga, imwani;Inu okondana, imwani kwambiri.2Ndinagona tulo koma mtima wanga unali maso.Tamverani, bwenzi langa akugogoda:“Nditsekulire, mlongo wanga, bwenzi langa,nkhunda yanga, wangwiro wanga.Mutu wanga wanyowa ndi mame,tsitsi langa lanyowa chifukwa cha nkhungu ya usiku.”3Ndavula kale zovala zanga,kodi ndizivalenso?Ndasamba kale mapazi angakodi ndiwadetsenso?4Bwenzi langa anapisa dzanja lake pa chibowo cha pa chitseko;mtima wanga unagunda chifukwa cha iye.5Ndinanyamuka kukamutsekulira wachikondi wangayo,ndipo manja anga anali noninoni ndi mure,zala zanga zinali mure chuchuchu,pa zogwirira za chotsekera.6Ndinamutsekulira wachikondi wanga,koma nʼkuti wachikondi wangayo atachoka; iye anali atapita.Mtima wanga unafumuka chifukwa cha kuchoka kwake.Ndinamuyangʼanayangʼana koma sindinamupeze.Ndinamuyitana koma sanandiyankhe.7Alonda anandipezapamene ankayendera mzindawo.Anandimenya ndipo anandipweteka;iwo anandilanda mwinjiro wanga,alonda a pa khoma aja!8Inu akazi a ku Yerusalemu ndithu ndikukupemphani,mukapeza wokondedwa wangayo,kodi mudzamuwuza chiyani?Muwuzeni kuti ine ndadwala nacho chikondi.9Iwe wokongola kuposa akazi onsewa,kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana wina aliyense bwanji?Kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana ena onse chotanikuti uzichita kutipempha motere?10Wokondedwa wangayo ndi wowala kwambiri ndi wathanzipakati pa anthu 1,000.11Mutu wake ndi golide woyengeka bwino;tsitsi lake ndi lopotanapotana,ndiponso lakuda bwino ngati khwangwala.12Maso ake ali ngati nkhundamʼmbali mwa mitsinje ya madzi,ngati nkhunda zitasamba mu mkaka,zitayima ngati miyala yamtengowapatali.13Masaya ake ali ngati timinda ta mbewu zokometsera zakudyazopatsa fungo lokoma.Milomo yake ili ngati maluwa okongolaamene akuchucha mure.14Manja ake ali ngati ndodo zagolidezokongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali.Thupi lake ndi losalala ngati mnyanga wanjovuwoyikamo miyala ya safiro.15Miyendo yake ili ngati mizati yamwala,yokhazikika pa maziko a golide.Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni,abwino kwambiri ngati mkungudza.16Milomo yake ndi yosangalatsa kwambiri;munthuyo ndi wokongola kwambiri!Uyu ndiye wachikondi wanga ndi bwenzi langa,inu akazi a ku Yerusalemu.