NYIMBO YA SOLOMONI3nya_bib
1Usiku wonse ndili pa bedi langandinafunafuna amene mtima wanga umamukonda;ndinamufunafuna koma osamupeza.2Ndikudzuka tsopano ndipo ndidzayendayenda mu mzinda,mʼmisewu yake ndi mʼmabwalo ake;ndidzamufunafuna amene mtima wanga umamukonda.Kotero ine ndinamufunafuna iyeyo koma osamupeza.3Alonda anandipezapamene ankayendera mzinda.“Kodi mwamuonako amene mtima wanga umamukonda?”4Nditawapitirira pangʼonondinamupeza amene mtima wanga umamukonda.Ndinamugwira ndipo sindinamulole kuti achokempaka nditamulowetsa mʼnyumba ya amayi anga,mʼchipinda cha amene anandibereka.5Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphanipali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo:Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsampaka pamene chifunire ichocho.6Kodi ndani amene akubwera kuchokera ku chipululungati utsi watolotolo,wonunkhira mure ndi lubani,zopangidwa kuchokera ku zonunkhira zonse za anthu amalonda?7Ona! Chimenecho ndi chonyamulira Solomoni,choperekezedwa ndi asilikali 60,anthu amphamvu a ku Israeli,8onse atanyamula lupanga,onse odziwa bwino nkhondo,aliyense ali ndi lupanga pambali pake,kukonzekera zoopsa za usiku.9Mfumu Solomoni anadzipangira chonyamulirachi;anachipanga ndi matabwa ochokera ku Lebanoni.10Milongoti yake anayipanga yasiliva,kumbuyo kwake kwa golide.Mipando yake inakutidwa ndi nsalu yapepo,anakongoletsa mʼkati mwake ndi chikondicha akazi a ku Yerusalemu.11Tukulani inu akazi a ku Ziyonindipo mudzaone mfumu Solomoni atavala chipewa chaufumu,chipewa chaufumu chimene amayi ake anamuvekapa tsiku la ukwati wake,tsiku limene mtima wake unasangalala.