MASALIMO99nya_bib
1Yehova akulamulira,mitundu ya anthu injenjemere;Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,dziko lapansi ligwedezeke.2Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.3Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,Iye ndi woyera.4Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamoInu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.5Kwezani Yehova Mulungu wathundipo mulambireni pa mapazi ake;Iye ndi woyera.6Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;iwo anayitana Yehovandipo Iyeyo anawayankha.7Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.8Inu Yehova Mulungu wathu,munawayankha iwo;Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.9Kwezani Yehova Mulungu wathundipo mumulambire pa phiri lake loyera,pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.