MASALIMO98nya_bib
Salimo.
1Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa;dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyerazamuchitira chipulumutso.2Yehova waonetsa chipulumutso chakendipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.3Iye wakumbukira chikondi chakendi kukhulupirika kwake pa Aisraeli;malekezero onse a dziko lapansi aonachipulumutso cha Mulungu wathu.4Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi,muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.5Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze,ndi zeze ndi mawu a kuyimba,6ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimunafuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.7Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.8Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo,mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;9izo ziyimbe pamaso pa Yehova,pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,ndi mitundu ya anthu mosakondera.