MASALIMO96nya_bib
1Imbirani Yehova nyimbo yatsopano;Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.2Imbirani Yehova, tamandani dzina lake;lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.3Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko,ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.4Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda;ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.5Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano,koma Yehova analenga mayiko akumwamba.6Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake,mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.7Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina,perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.8Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake;bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.9Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake;njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.10Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.”Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe;Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.11Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere;nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;12minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo.Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;13idzayimba pamaso pa Yehova,pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi;adzaweruza dziko lonse mwachilungamondi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.