MASALIMO93nya_bib
1Yehova akulamulira, wavala ulemerero;Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu,dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.2Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale;Inu ndinu wamuyaya.3Nyanja zakweza Inu Yehova,nyanja zakweza mawu ake;nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.4Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri,ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja,Yehova mmwamba ndi wamphamvu.5Malamulo anu Yehova ndi osasinthika;chiyero chimakongoletsa nyumba yanumpaka muyaya.