MASALIMO87nya_bib
Salimo la Ana a Kora.
1Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;2Yehova amakonda zipata za Ziyonikupambana malo onse okhalamo a Yakobo.3Za ulemerero wako zimakambidwa,Iwe mzinda wa Mulungu:Sela4“Ndidzanena za Rahabe ndi Babulonipakati pa iwo amene amandidziwa.Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”5Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,“Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”6Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:“Uyu anabadwira mʼZiyoni.”Sela7Oyimba ndi ovina omwe adzati,“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”