MASALIMO83nya_bib

Nyimbo. Salimo la Asafu.

1Inu Mulungu musakhale chete;musangoti phee, Mulungu musangoti duu.2Onani adani anu akuchita chiwawa,amene amadana nanu autsa mitu yawo.3Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu;Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.4Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewukuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”
5Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu;Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:6Matenti a Edomu ndi Aismaeli,Mowabu ndi Ahagiri,7Agebala, Aamoni ndi Aamaleki,Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.8Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawokupereka mphamvu kwa ana a Loti.Sela
9Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani,monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.10Amene anawonongedwa ku Endorindi kukhala ngati zinyalala.11Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebuana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna,12amene anati, “Tiyeni tilande dzikola msipu la Mulungu.”
13Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga,ngati mankhusu owuluka ndi mphepo.14Monga moto umatentha nkhalango,kapena malawi a moto kuyatsa phiri,15kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho,ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe.16Muphimbe nkhope zawo ndi manyazikuti adzafunefune dzina lanu Yehova.
17Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse;awonongeke mwa manyazi.18Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova,ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.