MASALIMO82nya_bib
Salimo la Asafu.
1Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu;Iye akuweruza pakati pa “milungu.”2“Mudzateteza osalungama mpaka liti,ndi kukondera anthu oyipa?3Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.4Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.5“Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse.Amayendayenda mu mdima;maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.6“Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu,nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’7Koma mudzafa ngati anthu wamba;mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”8Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.