MASALIMO70nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho.

1Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.2Iwo amene akufunafuna moyo wangaachititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;onse amene akukhumba chiwonongeko changaabwezedwe mopanda ulemu.3Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,”abwerere chifukwa cha manyazi awo.4Koma onse amene akufunafuna Inuakondwere ndi kusangalala mwa Inu;iwo amene amakonda chipulumutso chanunthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”
5Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;Inu Yehova musachedwe.