MASALIMO66nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo.

1Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!2Imbani ulemerero wa dzina lake;kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.3Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu!Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambirikotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.4Dziko lonse lapansi limaweramira inu;limayimba matamando kwa Inu;limayimba matamando pa dzina lanu.”Sela.
5Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.6Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma,iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi.Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.7Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya,maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina.Anthu owukira asadzitukumule.
8Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,mulole kuti mawu a matamando ake amveke;9Iye watchinjiriza miyoyo yathundi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.10Pakuti Inu Mulungu munatiyesa;munatiyenga ngati siliva.11Inu mwatilowetsa mʼndendendi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.12Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu;ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi,koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.
13Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopserezandi kukwaniritsa malumbiro anga.14Malumbiro amene milomo yanga inalonjezandi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.15Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inundi chopereka cha nkhosa zazimuna;ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi.Sela
16Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu.Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.17Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga,matamando ake anali pa lilime panga.18Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwangaAmbuye sakanamvera;19koma ndithu Mulungu wamvetserandipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.20Matamando akhale kwa Mulunguamene sanakane pemphero langakapena kuletsa chikondi chake pa ine!