MASALIMO63nya_bib
Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda.
1Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,moona mtima ine ndimakufunafunani;moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,thupi langa likulakalaka inu,mʼdziko lowuma ndi lotopetsakumene kulibe madzi.2Inu ndinakuonani ku malo anu opatulikandipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.3Chifukwa chikondi chanundi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.4Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.5Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.6Pa bedi panga ndimakumbukira inu;ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.7Chifukwa ndinu thandizo langa,ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.8Moyo wanga umakangamira Inu;dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.9Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa;adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.10Iwo adzaperekedwa ku lupangandi kukhala chakudya cha ankhandwe.11Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.