MASALIMO55nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya Davide. Pa zoyimbira za zingwe.

1Mvetserani pemphero langa, Inu Mulungu,musakufulatire kupempha kwanga,2mverani ndipo mundiyankhe.Maganizo anga akundisautsa ndipo ndathedwa nzeru3chifukwa cha mawu a adani anga,chifukwa cha kupondereza kwa anthu oyipa;pakuti andidzetsera masautsondipo akundizunza mu mkwiyo wawo.
4Mtima wanga ukupweteka mʼkati mwanga;mantha a imfa andigwera.5Mantha ndi kunjenjemera zandizinga;mantha aakulu andithetsa nzeru.6Ndinati, “Ndithu, ndikanakhala ndi mapiko ankhunda!Ndikanawulukira kutali ndi kukapuma.7Ndikanathawira kutalindi kukakhala mʼchipululu.8Ndikanathamangira kumalo anga a chitetezo;kutali ndi mphepo yaukali ndi yamkuntho.”
9Sokonezani maganizo a oyipa, Inu Ambuye, tsutsani mawu awo;pakuti ine ndikuona chiwawa ndi mkangano mu mzinda.10Usana ndi usiku iwo akuzungulirazungulira pa makoma ake;nkhwidzi ndi kuzunza kuli mʼkati mwake.11Mphamvu zowononga zili pa ntchito mu mzinda;kuopseza ndi mabodza sizichoka mʼmisewu yake.
12Akanakhala mdani akundinyoza, inendikanapirira;akanakhala mdani akudzikweza yekha kutsutsana nane,ndikanakabisala.13Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye,bwenzi langa la pondaapanʼpondepo, ndi amene ukuchita zimenezi.14Mnzanga amene nthawi ina tinkasangalalapa chiyanjano chokoma ku nyumba ya Mulungu.
15Mulole imfa itenge adani anga mwadzidzidzi;alowe mʼmanda ali amoyopakuti choyipa chili pakati pawo.
16Koma ine ndinafuwulira kwa Mulungu,ndipo Yehova anandipulumutsa.17Madzulo, mmawa ndi masanandimalira mowawidwa mtima,ndipo Iye amamva mawu anga.18Iye amandiwombola ine osavulazidwapa nkhondo imene yafika kulimbana nane,ngakhale kuti ndi ambiri amene akunditsutsa.19Mulungu amene ali pa mpando wake kwamuyaya,adzandimenyera nkhondo; adzawatsitsa adani anga,chifukwa safuna kusintha njira zawo zoyipandipo saopa Mulungu.
20Mnzanga woyenda naye wathira nkhondo abwenzi ake;iye akuphwanya pangano ake.21Mawu ake ndi osalala kuposa batalakomabe nkhondo ili mu mtima mwake;mawu ake ndi osalala kwambiri kuposa mafuta,komatu mawuwo ndi malupanga osololoka.
22Tulani nkhawa zanu kwa Yehovandipo Iye adzakulimbitsani;Iye sadzalola kuti wolungama agwe.23Koma Inu Mulungu mudzawatsitsa anthu oyipakulowa mʼdzenje lachiwonongeko;anthu okhetsa magazi ndi anthu achinyengosadzakhala moyo theka la masiku awo,koma ine ndimadalira Inu.