MASALIMO54nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.”

1Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu;onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.2Imvani pemphero langa, Inu Mulungumvetserani mawu a pakamwa panga.
3Alendo akundithira nkhondo;anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga,anthu amene salabadira za Mulungu.
4Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa;Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.
5Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe;mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.
6Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu;ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova,pakuti ndi labwino.7Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse,ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.