MASALIMO53nya_bib
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide.
1Chitsiru chimati mu mtima mwake,“Kulibe Mulungu.”Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa;palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.2Mulungu kumwamba amayangʼana pansi panopa ana a anthukuti aone ngati alipo wina wanzeru,wofunafuna Mulungu.3Aliyense wabwerera,iwo onse pamodzi akhala oyipa;palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino,ngakhale mmodzi.4Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi;anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi,ndipo sapemphera kwa Mulungu?5Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulupamene panalibe kanthu kochititsa mantha.Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo;inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.6Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni!Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake,lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!