MASALIMO52nya_bib
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, ndakatulo ya Davide; pamene Doegi Mwedomu anapita kwa Sauli ndi kunena kuti “Davide wapita ku nyumba ya Ahimeleki.”
1Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu?Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse,iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?2Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena;lilime lako lili ngati lumo lakuthwa,ntchito yako nʼkunyenga.3Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi.Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona.Sela4Umakonda mawu onse opweteka,iwe lilime lachinyengo!5Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya:iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako;iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.6Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha;adzamuseka nʼkumanena kuti,7“Pano tsopano pali munthuamene sanayese Mulungu linga lake,koma anakhulupirira chuma chake chambirinalimbika kuchita zoyipa!”8Koma ine ndili ngati mtengo wa oliviwobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu;ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungukwa nthawi za nthawi.9Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita;chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezerapakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.