MASALIMO50nya_bib

Salimo la Asafu.

1Wamphamvuyo, Yehova Mulungu,akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansikuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.2Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiriMulungu akuwala.3Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete;moto ukunyeketsa patsogolo pake,ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho4Iye akuyitanitsa zamumlengalengandi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.5Mundisonkhanitsire okhulupirika anga,amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.6Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake,pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.
7Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula,iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa;ndine Mulungu, Mulungu wako.8Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako,kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.9Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lakokapena mbuzi za mʼkhola lako,10pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yangandiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.11Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapirindiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga.12Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani,pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga.13Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimunakapena kumwa magazi a mbuzi?14“Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu,kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba.15Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso;Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”16Koma kwa woyipa, Mulungu akuti,“Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo angakapena kutenga pangano langa pa milomo yako?17Iwe umadana ndi malangizo angandipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.18Ukaona wakuba umamutsatira,umachita maere ako pamodzi ndi achigololo19Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipandipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo.20Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wakondipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni.21Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete;umaganiza kuti ndine wofanana nawekoma ndidzakudzudzulandipo ndidzakutsutsa pamaso pako.
22“Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungukuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:23Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza,ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetsechipulumutso cha Mulungu.”