MASALIMO47nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

1Ombani mʼmanja, inu anthu onse;fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.2Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!3Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;anayika anthu pansi pa mapazi athu.4Iye anatisankhira cholowa chathu,chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.Sela
5Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.6Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.
7Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;imbirani Iye salimo la matamando.8Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.9Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhanamonga anthu a Mulungu wa Abrahamu,pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;Iye wakwezedwa kwakukulu.