MASALIMO40nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Mofatsa ndinadikira YehovaIye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.2Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko,mʼthope ndi mʼchithaphwi;Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwendipo anandipatsa malo oyimapo olimba.3Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga.Ambiri adzaona,nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.
4Ndi wodala munthuamakhulupirira Yehova;amene sayembekezera kwa odzikuza,kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.5Zambiri, Yehova Mulungu wanga,ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita.Zinthu zimene munazikonzera ifepalibe amene angathe kukuwerengerani.Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera,zidzakhala zambiri kuzifotokoza.
6Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna,koma makutu anga mwawatsekula;zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimoInu simunazipemphe.7Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera.Mʼbuku mwalembedwa za ine.8Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga;lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”
9Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu;sinditseka milomo yangamonga mukudziwa Inu Yehova.10Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga;ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanupa msonkhano waukulu.
11Musandichotsere chifundo chanu Yehova;chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.12Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira;machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona.Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga,ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga.
13Pulumutseni Yehova;Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.14Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wangaachititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;onse amene amakhumba chiwonongeko changaabwezedwe mwamanyazi.15Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!”abwerere akuchita manyazi.16Koma iwo amene amafunafuna Inuakondwere ndi kusangalala mwa Inu;iwo amene amakonda chipulumutso chanunthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!”
17Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa;Ambuye andiganizire.Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga;Inu Mulungu wanga, musachedwe.