MASALIMO39nya_bib

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide.

1Ndinati, “Ndidzasamalira njira zangandipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekereronthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”2Koma pamene ndinali cheteosanena ngakhale kanthu kalikonse kabwinomavuto anga anachulukirabe.3Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga,ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka;kenaka ndinayankhula ndi lilime langa:
4“Yehova ndionetseni mathero a moyo wangandi chiwerengero cha masiku anga;mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.5Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.Sela6Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:Iye amangovutika koma popanda phindu;amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.
7“Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?Chiyembekezo changa chili mwa Inu.8Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;musandisandutse chonyozeka kwa opusa.9Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa pangapakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.10Chotsani mkwapulo wanu pa ine;ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.11Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo;mumawononga chuma chawo monga njenjete;munthu aliyense ali ngati mpweya.Sela
12“Imvani pemphero langa Inu Yehova,mverani kulira kwanga kopempha thandizo;musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu,popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa;monga anachitira makolo anga onse.13Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalalandisanafe ndi kuyiwalika.”