MASALIMO32nya_bib
Salimo la Davide. Malangizo.
1Ngodala munthuamene zolakwa zake zakhululukidwa;amene machimo ake aphimbidwa.2Ngodala munthuamene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iyendipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.3Pamene ndinali chete,mafupa anga anakalambachifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.4Pakuti usana ndi usikudzanja lanu linandipsinja;mphamvu zanga zinathamonga nthawi yotentha yachilimwe.Sela5Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,sindinabise mphulupulu zanga.Ndinati, “Ine ndidzawululazolakwa zanga kwa Yehova,ndipo Inu munandikhululukiramlandu wa machimo anga.”Sela6Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyopomwe mukupezeka;ndithu pamene madzi amphamvu auka,sadzamupeza.7Inu ndi malo anga obisala;muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizingandi nyimbo zachipulumutso.Sela8Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.9Usakhale ngati kavalo kapena bulu,zimene zilibe nzeru,koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.10Zowawa ndi zambiri za anthu oyipakoma chikondi chosatha cha Yehovachimamuzinga munthu amene amadalira Iye.11Kondwerani mwa Yehova inu olungama;imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!