MASALIMO28nya_bib

Salimo la Davide.

1Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa;musakhale osamva kwa ine.Pakuti mukapitirira kukhala chete,ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.2Imvani kupempha chifundo kwangapomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize,pomwe ndikukweza manja angakuloza ku malo anu oyeretsetsa.
3Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa,pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa,amene amayankhula mwachikondi ndi anzawokoma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.4Muwabwezere chifukwa cha zochita zawondi ntchito zawo zoyipa;abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achitandipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.5Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova,ndi zimene manja ake anazichita,Iye adzawakhadzulandipo sadzawathandizanso.
6Matamando apite kwa Yehova,popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.7Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwendipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
8Yehova ndi mphamvu ya anthu ake,linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.9Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.