MASALIMO2nya_bib

1Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu?Akonzekeranji zopanda pake anthu?2Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;ndipo olamulira asonkhana pamodzikulimbana ndi Ambuyendi wodzozedwa wakeyo.3Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awondipo titaye zingwe zawo.”
4Wokhala mmwamba akuseka;Ambuye akuwanyoza iwowo.5Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wakendi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,6“Ine ndakhazikitsa mfumu yangapa Ziyoni, phiri langa loyera.”7Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula:Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga;lero Ine ndakhala Atate ako.8Tandipempha,ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako;malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.9Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo;udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”
10Kotero, inu mafumu, chenjerani;chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.11Tumikirani Yehova mwa manthandi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.12Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye;kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu,pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa.Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.